Ezekiel 45:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pomadzagaŵa dziko kuti fuko lililonse lilandire chigawo chake, chimodzi adzachipatule kuti chidzakhale cha Chauta. M'litali mwake mudzakhale makilomita 12 ndi theka, muufupi mwake khumi. Malo onsewo adzakhala opatulika.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo pogawa dziko likhale cholowa chao, mupereke chopereka kwa Yehova, ndicho gawo lopatulika la dziko; m'litali mwake likhale la mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwake mikono zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ake onse pozungulira pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mukamadzagawa dziko kuti fuko lililonse lilandire cholowa chake, mudzapatuleko chigawo chimodzi kuti chikhale cha Yehova. Mulitali mwake mudzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka ndipo mulifupi mwake makilomita khumi. Malo onsewo adzakhale opatulika.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo pogawa dziko likhale calowa cao, mupereke copereka kwa Yehova, ndico gawo lopatulika la dziko; m'litali mwace likhale la mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu, ndi kupingasa kwace zikwi makumi awiri; likhale lopatulika m'malire ace onse pozungulira pace.