Ezekiel 45:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Mupereke nkhosa imodzi pa gulu la nkhosa 200 za m'mabusa abwino a Israele. Ndimo m'mene mudzaperekere nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndiponso nsembe zachiyanjano, kupepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi mwanawankhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wochokera kumadimba a Israele, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwachitira chotetezera, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muperekenso nkhosa imodzi pa gulu lankhosa 200 za pa msipu wabwino wa mu Israeli. Izi zidzagwiritsidwa ntchito monga nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano ndi nsembe zopepesera milandu ya anthu. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi mwana wa nkhosa mmodzi wa zoweta, kumtenga pa mazana awiri wocokera ku madimba a Israyeli, ndiye wa nsembe yaufa, ndi wa nsembe yopsereza, ndi wa nsembe zoyamika, kuwacitira cotetezera, ati Ambuye Yehova.