Ezekiel 45:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ndipo mfumu izipereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe zatirigu ndi nsembe zazakumwa pa masiku achikondwerero, ndi a pokhala mwezi, masiku a Sabata, ndiponso pa masiku ena amene Aisraele amaŵasunga. Mfumuyo ipereke zofunikira ku nsembe zopepesera machimo, nsembe zatirigu, nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, kuti zonsezo zikhale zopepesera machimo a Aisraele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Udzakhala udindo wa mfumu kupereka zofunikira ku nsembe zopsereza, nsembe za chakudya, ndi nsembe za zakumwa pa nthawi ya zikondwerero, chikondwerero cha mwezi watsopano ndi cha masabata, nthawi yonse ya zikondwerero zoyikika za Aisraeli. Mfumuyo idzapereka nsembe zopepesera machimo, nsembe za chakudya, nsembe zopsereza, ndi nsembe zachiyanjano kuti zikhale nsembe zopepesera machimo a Aisraeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pamadyerero, ndi pokhala mwezi, ndi pamasabata; pa madyerero onse oikika a nyumba ya Israyeli; ndipo apereke nsembe yaucimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kucitira cotetezera nyumba ya Israyeli.