Ezekiel 45:19 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo, ndipo aŵapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinai za pamwamba pa guwa ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo lam'kati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yauchimo, naupake pa mphuthu za Kachisi, ndi pangodya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za chipata cha bwalo lam'kati.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Wansembe atengeko magazi a nsembe yopepesera machimoyo ndipo awapake pa mphuthu za Nyumba ya Mulungu, pa ngodya zinayi za pamwamba pa guwa lansembe ndi pa mphuthu za pa chipata cha bwalo la mʼkati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo wansembe atengeko mwazi wa nsembe yaucimo, naupake pa mphuthu za kacisi, ndi pa ngondya zinai za phaka la guwa la nsembe, ndi pa mphuthu za cipata ca bwalo lam'kati.