Ezekiel 45:23 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa masiku asanu ndi aŵiri a chikondwererocho, mfumuyo izipereka kwa Chauta nsembe izi zopsereza: ng'ombe zamphongo zisanu ndi ziŵiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziŵiri, zonsezo zopanda chilema. Tsiku lililonse iziperekanso nsembe ya tonde mmodzi, kupepesera machimo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo masiku asanu ndi awiri a chikondwerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda chilema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yauchimo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa masiku asanu ndi awiri a chikondwererocho, mfumu ipereke kwa Yehova nsembe zopsereza izi: ngʼombe zazimuna zisanu ndi ziwiri, nkhosa zazimuna zisanu ndi ziwiri, zonsezi zopanda chilema. Pa masikuwa mfumu iziperekanso mbuzi imodzi yayimuna ngati nsembe yopepesera machimo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo masiku asanu ndi awiri a madyerero akonzere Yehova nsembe yopsereza, ng'ombe zisanu ndi ziwiri, ndi nkhosa zamphongo zisanu ndi ziwiri zopanda cirema, tsiku ndi tsiku, masiku asanu ndi awiriwa; ndi tonde tsiku ndi tsiku, akhale wa nsembe yaucimo.