Ezekiel 45:25 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono mfumu ichitenso chimodzimodzi pa tsiku la khumi ndi chisanu la mwezi wachisanu ndi chiŵiri. Chikondwerero chimenecho chizichitika masiku asanu ndi aŵiri. Izipereka nsembe za mtundu womwewonso, zopepesera machimo, nsembe zopsereza, ndiponso nsembe zaufa ndi zamafuta zomwe.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Mwezi wachisanu ndi chiwiri, tsiku lakhumi ndi chisanu la mwezi, pachikondwerero, achite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yauchimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Pa nthawi ya chikondwerero cha masiku asanu ndi awiri, chimene chimayamba pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, mfumuyo iziperekanso nsembe za mtundu womwewo: nsembe zopepesera machimo, nsembe zopsereza, nsembe za chakudya ndi za mafuta.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Mwezi wacisanu ndi ciwiri, tsiku lakhumi ndi cisanu la mwezi, pamadyerero, acite momwemo masiku asanu ndi awiri, monga mwa nsembe yaucimo, monga mwa nsembe yopsereza, ndi monga mwa nsembe yaufa, ndi monga mwa mafuta.