Ezekiel 45:4 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malo ameneŵa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Chauta pomutumikira. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zao ndi Nyumba ya Mulungu yomwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a kwa malo opatulika.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malo opatulika amenewa adzakhalanso a ansembe amene amatumikira ku malo opatulika, amene amayandikira Yehova kuti amutumikire. Pamenepo padzakhala malo omangapo nyumba zawo ndi malo omangapo Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndilo gawo lopatulika la dziko, ndilo la ansembe atumiki a malo opatulika, amene ayandikira kutumikira Yehova; apo ndipo amange nyumba zao, likhale malo a pa okha a: kwa malo opatulika.