Ezekiel 45:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi chigawo china cha makilomita 12 ndi theka m'litali mwake, ndi makilomita asanu muufupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhalenso midzi yao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndilo gawo la Alevi, atumiki a Kachisi; likhale laolao la midzi yokhalamo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Alevi otumikira ku Nyumba ya Mulungu adzakhala ndi malo a makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake ndi makilomita asanu mulifupi mwake. Kumeneko ndiko kudzakhale midzi yawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, ndi zikwi khumi kupingasa kwace, ndilo gawo la Alevi, atumiki a kacisi; likhale lao lao la midzi yokhalamo.