Ezekiel 45:6 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Poyandikana ndi malo opatulikawo, musankhe kadziko kokwanira makilomita aŵiri ndi theka muufupi mwake, m'litali mwake makilomita 12 ndi hafu, kuti akhale malo a mzinda. Malo ameneŵa adzakhala a banja lonse la Israele.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo dziko lake la mudziwo mulipereke la mikono zikwi zisanu kupingasa kwake, ndi mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, pa mbali ya chipereko chopatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Moyandikana ndi malo opatulika, padzakhale malo a makilomita awiri ndi theka mulifupi mwake ndi makilomita khumi ndi awiri ndi theka mulitali mwake; kuti akhale malo a mzinda. Malo amenewa adzakhala a Aisraeli onse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo dziko lace la mudziwo mulipereke la zikwi zisanu kupingasa kwace, ndi zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, pa mbali ya cipereko copatulika, ndilo la nyumba yonse ya Israyeli.