Ezekiel 45:7 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mupatulenso dera la mfumu. Likhudzane ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda, liyandikane ndi zigawozo chakuzambwe ndi chakuvuma. Litalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israele, mpaka kukafika ku malire a dziko kuzambwe ndi kuvuma.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lake mbali ina ndi mbali inzake ya chipereko chopatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa chipereko chopatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa; ndi m'litali mwake mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira kumalire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Mfumu idzakhale ndi malo okhudzana ndi chigawo cha malo opatulika ndi cha mzinda. Malowo ayandikane ndi zigawozo chakummawa ndi chakumadzulo. Malowo atalike ngati chigawo chimodzi cha fuko la Israeli kuyambira ku malire akummawa mpaka ku malire akumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kalonga adzakhala nalo gawo lace mbali yina ndi mbali inzace ya cipereko copatulika, ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa cipereko copatulika, ndi kutsogolo kwa dziko la mudzi, mbali ya kumadzulo kumadzulo, ndi mbali ya kum'mawa kum'mawa; ndi m'litali mwace mudzalingana ndi limodzi la magawo, kuyambira ku malire a kumadzulo kufikira malire a kum'mawa.