Ezekiel 45:8 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Deralo lidzakhala choloŵa cha mfumu m'dziko la Israele. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma azidzaŵalola Aisraele kuti akhale ndi zigawo zaozao.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'dzikomo ili lidzakhala lakelake m'Israele; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israele monga mwa mafuko ao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Malowa adzakhala chigawo cha mfumu mu Israeli. Choncho mafumu anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzidzalola Aisraeli kuti akhale ndi zigawo zawozawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'dzikomo ili lidzakhala lace lace m'Israyeli; ndipo akalonga anga sadzazunzanso anthu anga, koma adzapereka dziko kwa nyumba ya Israyeli monga mwa mapfuko ao.