Ezekiel 45:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Tsono pakwana, inu olamulira a ku Israele. Lekani nkhanza ndi kuzunza anthu. Muzimvera malamulo ndipo muzichita zachilungamo. Alekeni anthu anga, musamaŵachotsa pa dziko lao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Tsono pakwana, inu akalonga a Israeli. Lekani nkhanza zanu ndi kupondereza anthu anga. Muzitsata chilungamo ndi kuchita zokomera anthu. Musapirikitse anthu anga mʼdzikomo. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israyeli inu, lekani kucita ciwawa, ndi kulanda za eni ace; mucite ciweruzo ndi cilungamo; lekani kupitikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.