Ezekiel 46:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Chipata chakuvuma cha bwalo lam'kati chizikhala chotseka masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito. Azitsekula pa tsiku la Sabata lokha ndi tsiku limene mwezi wakhala.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Pa chipata cha bwalo lam'kati choloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ambuye Yehova akuti, Chipata chakummawa cha bwalo lamʼkati chizikhala chotseka pa masiku asanu ndi limodzi ogwira ntchito, koma chizitsekulidwa pa tsiku la sabata ndi pa tsiku la chikondwerero cha mwezi watsopano.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Pa cipata ca bwalo lam'kati coloza kum'mawa patsekedwe masiku asanu ndi limodzi ogwira nchito; koma tsiku la Sabata patsegulidwe, ndi tsiku lokhala mwezi patsegulidwe.