Ezekiel 46:11 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za ufa zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ng'ombe yamphongo iliyonse, efa imodzinso pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, koma pa mwanawankhosa azipereka monga m'mene angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi pazikondwerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Pa masiku achikondwerero ndi pa masiku ena osankhidwa, zopereka za chakudya zikhale zokwanira efa imodzi pamodzi ndi ngʼombe yayimuna iliyonse, efa imodzinso ndi nkhosa yayimuna, koma pa mwana wankhosa apereke monga angathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi pamadyerero, ndi pa masiku opatulika, nsembe yaufa ikhale ya efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.