Ezekiel 46:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamene mfumu ikufuna kupereka zaufulu kwa Chauta, monga nsembe yopsereza kapena nsembe zachiyanjano, aitsekulire chipata chakuvuma. Ipereke nsembe yake yopsereza ndi nsembe yake yachiyanjano, monga m'mene imachitira pa tsiku la Sabata. Itamaliza, ituluke. Itatuluka, chipata chitsekedwe.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kalonga akapereka chopereka chaufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa chipata choloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yake yopsereza, ndi nsembe zake zoyamika, monga umo amachitira tsiku la Sabata; atatero atuluke; ndipo atatuluka, wina atseke pachipata.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamene mfumu ikufuna kupereka chopereka chaufulu kwa Yehova, kaya ndi nsembe yopsereza kapena zopereka za chiyanjano, ayitsekulire chipata chakummawa. Iyo ipereke nsembe yopsereza kapena zopereka zake za chiyanjano monga imachitira pa tsiku la Sabata. Kenaka ituluke ndipo mfumuyo itatuluka, atseke chitsekocho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kalonga akapereka copereka caufulu nsembe yopsereza, kapena nsembe zoyamika kwa Yehova, amtsegulire pa cipata coloza kum'mawa; ndipo azipereka nsembe yace yopsereza, ndi nsembe zace zoyamika, monga umo amacitira tsiku la Sabata; atatero aturuke; ndipo ataturuka, wina atseke pacipata.