Ezekiel 46:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso m'maŵa mulimonse ufa wokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Nsembe imeneyi yopereka kwa Chautayi iziperekedwa nthaŵi zonse.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Uperekenso nsembe yaufa pamodzi naye m'mawa ndi m'mawa, limodzi la magawo asanu ndi limodzi la efa, ndi limodzi la magawo atatu la hini wa mafuta, kusanganiza ndi ufa wosalala, ndiyo nsembe yaufa ya Yehova kosalekeza, mwa lemba losatha.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi nyamayo aziperekanso mmawa uliwonse chopereka cha chakudya chokwanira chimodzi mwa zigawo zisanu ndi chimodzi za efa. Aziperekanso chimodzi mwa zigawo zitatu za hini ya mafuta okandira ufa wosalala. Chopereka cha chakudya chimenechi chiziperekedwa kwa Yehova nthawi zonse mwa lamulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika