Ezekiel 46:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Kalonga akapereka chigawo cha chuma chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo ndi ya ana akewodi, popeza kuti ndi chigawo cha choloŵa cha makolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wake wina wamwamuna mphatso idzakhala cholowa chake, ndicho chaochao cha ana ake, cholowa chao.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“ ‘Ine Ambuye Yehova ndikuti: Ngati kalonga apereka mphatso chigawo cha cholowa chake kwa mmodzi mwa ana ake, mphatsoyo idzakhala ya ana akewo. Idzakhala yawo chifukwa ndi cholowa chawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Kalonga akapatsa mwana wace wina wamwamuna mphatso idzakhala colowa cace, ndico cao cao ca ana ace, colowa cao.