Ezekiel 46:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Koma akapereka mphatso yotere kwa mmodzi mwa atumiki ake, idzakhala ya mtumikiyo mpaka pa chaka cha ufulu. Pamenepo mphatsoyo idzabwerera kwa kalonga uja, chifukwa chuma chake chonse ncha ana okha.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma akapatsa mphatso yotenga kucholowa chake kwa wina wa anyamata ake, idzakhala yake mpaka chaka cha ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma cholowa chake chikhale cha ana ake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Koma ngati ipereka mphatso yotere kuchokera pa cholowa chake kwa mmodzi mwa antchito ake, mphatsoyo idzakhala ya wantchitoyo mpaka chaka chaufulu. Pambuyo pake idzabwereranso kwa kalongayo chifukwa cholowa chake ndi cha ana ake.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma akapatsa mphatso yotenga ku colowa cace kwa wina wa anyamata ace, idzakhala yace mpaka caka ca ufulu; pamenepo ibwerere kwa kalonga, koma colowa cace cikhale ca ana ace.