Ezekiel 46:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono kalonga asalande anthu gawo la chuma chaochao pakuŵachotsa m'dera lao la dziko. Ana ake kalonga aŵapatse choloŵa chao pa dziko limene lili lakelake, kuti choncho asalande ndi mmodzi yemwe mwa ana anga choloŵa chake.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kalonga asatengeko cholowa cha anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko laolao; apatse ana ake cholowa kulemba dziko lakelake, kuti anthu anga asabalalike, yense kuchoka m'dziko lake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kalonga asalande cholowa chilichonse cha anthu, kuwachotsa mʼdera lawo la dziko. Iye apereke kwa ana ake cholowa chawo chochokera pa chuma chakechake, kuti pasapezeke ndi mmodzi yemwe mwa anthu anga wolandidwa chuma chake.’ ”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kalonga asatengeko colowa ca anthu kuwazunza, ndi kulanda dziko lao lao; apatse ana ace colowa kulemba dziko lace lace, kuti anthu anga asabalalike, yense kucoka m'dziko lace.