Ezekiel 46:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Aŵa ndi malo m'mene ansembe azidzaphikiramo nyama za nsembe zopepesera kupalamula ndiponso nsembe zopepesera machimo. Kumenekonso ndiko kumene azidzaotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi m'bwalo lakunja kuwopa kuti angapatsireko kuyera anthu enawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yopalamula, ndi nsembe yauchimo; kumenenso aziocha mikate ya ufa wa nsembe, kuti asatuluke nazo kubwalo lakunja ndi kupatulika kwambiri anthu,
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo anandiwuza kuti, “Awa ndi malo amene ansembe adzaphikirapo nsembe yopepesera kupalamula ndi nsembe yopepesera machimo. Kumenekonso azidzawotcherako chopereka cha chakudya. Sadzatuluka nazo zoyerazi mʼbwalo lakunja kuopa kuti angapatsireko kuyera anthu ena.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anati kwa ine, Pano ndipo ansembe aziphikira nsembe yoparamula, ndi nsembe yaucimo; kumenenso azioca mikate ya ufa wa nsembe, kuti asaturuke nazo ku bwalo lakunja ndi kupatulikitsa anthu,