Ezekiel 46:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Atatero adandiloŵetsa m'bwalo lakunja napita nane ku ngodya zinai za bwalolo. Tsono m'kati mwa ngodya iliyonse munali bwalo lina.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatulukira nane kubwalo lakunja, nandipititsa kungodya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngodya monse munali bwalo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pambuyo pake anandilowetsa mʼbwalo lakunja napita nane ku ngodya zinayi za bwalolo. Ndipo ndinaona mʼkati mwa ngodya iliyonse bwalo lina.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaturukira nane ku bwalo lakunja, nandipititsa ku ngondya zinai za bwaloli; ndipo taonani, m'ngondya monse munali bwalo.