Ezekiel 46:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero pa ngodya zinai za bwalo lalikululo panali mabwalo ena ang'onoang'ono. Mabwalo amenewo anali ofanana, m'litali mwake mamita makumi aŵiri, muufupi mwake mamita khumi ndi asanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
M'ngodya zinai za bwalo munali mabwalo ochingika, m'litali mwake mikono makumi anai, kupingasa kwake makumi atatu; awa anai m'ngodyazi analingana muyeso wake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero pa ngodya zinayi za bwalo panalinso mabwalo ena angʼonoangʼono. Mabwalo amenewa anali ofanana. Mulitali mwake munali mamita makumi awiri ndipo mulifupi mwake munali mamita khumi ndi asanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
M'ngondya zinai za bwalo munali mabwalo ocingika, m'litali mwace mikono makumi anai, kupingasa kwace makumi atatu; awa anai m'ngondyazi analingana muyeso wace.