Ezekiel 46:5 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pamodzi ndi nkhosa yamphongo iliyonse, mfumu izipereka ufa wokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi anaankhosa aja mfumu iziperekanso ufa monga ingathere. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya ufa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa anaankhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini wa mafuta wa paefa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pamodzi ndi nkhosa yayimuna, mfumu izipereka nsembe ya chakudya yokwanira efa imodzi. Pamodzi ndi ana ankhosa, mfumu izipereka monga ikufunira kutero. Iperekenso hini imodzi ya mafuta pa efa iliyonse ya tirigu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi nsembe yaufa ikhale efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi nsembe ya ufa wa pa ana a nkhosa, monga akhoza kupatsa; ndi hini a wa mafuta wa paefa.