Ezekiel 46:6 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pa tsiku limene mwezi wakhala mfumu ipereke mwanawang'ombe wamphongo wopanda chilema, anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zonsezo zopanda chilema.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwanawang'ombe wopanda chilema, ndi anaankhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda chilema;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Pa tsiku la mwezi watsopano mfumuyo ipereke mwana wangʼombe wamwamuna, ana ankhosa asanu ndi mmodzi ndiponso nkhosa yayimuna, zonsezi zopanda chilema.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo nsembe ya tsiku lokhala mwezi ikhale mwana wa ng'ombe wopanda cirema, ndi ana a nkhosa asanu ndi mmodzi, ndi nkhosa yamphongo, zikhale zopanda cirema;