Ezekiel 46:7 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Ipereke efa imodzi ya ufa pa ng'ombe yamphongo iliyonse, ndiponso efa ina pa nkhosa yamphongo iliyonse. Pa anaankhosa iperekenso ufa monga m'mene ingathere. Pamodzi ndi efa iliyonse ya ufa, ipereke hini imodzi ya mafuta.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa anaankhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ipereke efa imodzi ya tirigu pa ngʼombe yayimuna iliyonse ndiponso efa ina pa nkhosa yayimuna iliyonse. Pa ana ankhosa ipereke tirigu monga ikufunira kutero. Pamodzi ndi efa ya tirigu, ipereke hini imodzi ya mafuta.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndipo akonze nsembe yaufa, efa wa pa ng'ombe, ndi efa wa pa nkhosa yamphongo, ndi pa ana a nkhosa, monga akhoza; ndi hini wa mafuta wa paefa.