Ezekiel 46:9 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Pa masiku achikondwerero, anthu am'dzikomo akabwera kudzapembedza Chauta, munthu woloŵera pa chipata chakumpoto azidzatulukira pa chipata chakumwera. Munthu woloŵera pa chipata chakumwera, azidzatulukira pa chipata chakumpoto. Munthu aliyense asadzatulukire pomwe waloŵera, koma azipita chakutsogolo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'zikondwerero zoikika, iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumpoto kudzalambira, atulukire njira ya kuchipata cha kumwera; ndi iye amene alowera njira ya kuchipata cha kumwera, atulukire njira ya kuchipata cha kumpoto; asabwerere njira ya chipata anadzeracho, koma atulukire m'tsogolo mwake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Anthu a mʼdzikomo akabwera kudzapembedza Yehova pa masiku a chikondwerero, ngati munthu alowera pa chipata chakumpoto atulukire chipata chakummwera. Munthu wolowera chipata chakummwera, atulukire chipata chakumpoto. Munthu asatulukire pomwe walowera, koma atulukire pa chipata choyangʼanana nacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Koma pofika anthu a m'dziko pamaso pa Yehova m'madyerero oikika, iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumpoto kudzalambira, aturukire njira ya ku cipata ca kumwera; ndi iye amene alowera njira ya ku cipata ca kumwera, aturukire njira ya ku cipata ca kumpoto; asabwerere njira ya cipata anadzeraco, koma aturukire m'tsogolo mwace.