Ezekiel 47:1 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono munthu uja adabwerera nane ku chipata cha ku Nyumba ya Mulungu. Ndidaona kasupe akutuluka kunsi kwa chiwundo choloŵera ku Nyumba ya Mulungu chakuvuma, poti Nyumbayo inali yoyang'ana kuvuma. Kunkayenda madzi kunsi kwa chipupa chakumwera cha Nyumba ya Mulungu, chakumwera kwa guwa.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa chiundo cha nyumba kum'mawa; pakuti khomo lake la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kuchokera pansi pa nyumba, kumbali ya lamanja lake, kumwera kwa guwa la nsembe.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Munthuyo anabwerera nane ku chipata cha Nyumba ya Mulungu. Ndinaona madzi akutuluka kunsi kwa chiwundo cha Nyumba ya Mulungu chakummawa; poti Nyumba ya Mulungu inayangʼana kummawa. Madziwo ankachokera kunsi kwa mbali yakummwera ya Nyumba ya Mulungu; kummwera kwa guwa lansembe.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo anandibwezera ku khomo la nyumba, ndipo taonani, panatumphuka madzi pansi pa ciundo ca nyumba kum'mawa; pakuti khomo lace la nyumba linaloza kum'mawa; ndipo madzi anatsika kucokera pansi pa nyumba, ku mbali ya lamanja lace, kumwela kwa guwa la nsembe.