Ezekiel 47:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Asodzi a nsomba adzakhala pa madooko ao, chifukwa kuyambira ku Engedi mpaka ku Enegilaimu kudzakhala malo abwino oponyako akombe. Mumtsinjewo mudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga za m'Nyanja Yaikulu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Enegilaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundumitundu, ngati nsomba za m'Nyanja Yaikulu, zambirimbiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Asodzi adzayima mʼmbali mwa Nyanja Yakufa. Pakuti kuchokera ku Eni-Gedi mpaka ku Eni Egilaimu kudzakhala malo oponyako makoka. Kudzakhala nsomba zamitundumitundu, monga nsomba za ku Nyanja Yayikulu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika, kuti asodzi adzaima komweko; kuyambira pa Engedi kufikira ku Eneglaimu kudzakhala poyanikira makoka; nsomba zao zidzakhala za mitundu mitundu, ngati nsomba za m'nyanja yaikuru, zambirimbiri.