Ezekiel 47:12 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Pambali pa mtsinjewo, pa gombe lililonse, padzakhala mitengo yobereka zipatso za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota, ndipo zipatso zake zidzakhala zosalekeza. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake ndi ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya, ndipo masamba ake azidzachita mankhwala.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kumtsinje, kugombe kwake tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uliwonse wa chakudya, osafota tsamba lake, zipatso zake zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ake atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zake zidzakhala chakudya, ndi tsamba lake lakuchiritsa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mʼmbali zonse za mtsinje mudzamera mitengo ya zipatso zakudya za mtundu uliwonse. Masamba ake sadzafota kapena kulephera kubereka zipatso. Izidzabereka mwezi uliwonse, chifukwa madzi ake adzakhala ochokera ku Nyumba ya Mulungu. Zipatso zake anthu azidzadya ndipo masamba ake azidzachitira mankhwala.”
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kumtsinje, kugombe kwace tsidya lino ndi lija, kudzamera mtengo uli wonse wa cakudya, osafota tsamba lace, zipatso zace zomwe zosasowa; idzabala zipatso zatsopano mwezi ndi mwezi, popeza madzi ace atumphuka m'malo opatulika; ndi zipatso zace zidzakhala cakudya, ndi tsamba lace lakuciritsa.