Ezekiel 47:13 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Zimene Ambuye Chauta akunena ndi izi, akuti, “Naŵa malire amene mudzatsate poŵagaŵira dziko la Israele mafuko khumi ndi aŵiri aja: Yosefe alandire zigawo ziŵiri.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale cholowa chao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israele ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ambuye Yehova akuti, “Nawa malire amene mudzatsate powagawira dziko mafuko khumi ndi awiri a Israeli aja. Yosefe adzalandire zigawo ziwiri.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Atero Ambuye Yehova, Malire amene mugawe nao dziko likhale colowa cao monga mwa mafuko khumi ndi awiri a Israyeli ndi awa: Yosefe akhale nao magawo awiri.