Ezekiel 47:14 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dzikoli mudzagaŵana mofanana, chifukwa ndidalumbira kuti ndidzalipereka kwa makolo anu ndipo lidzakhala lanulanu. Motero lidzapatsidwa kwa inu mwamaere, kuti likhale choloŵa chanu.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudzakhala nalo cholowa chanu wina ndi mnzake yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani cholowa chanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mudzawagawire dzikolo mofanana. Paja ndinalumbira kwa makolo anu kuti dzikoli lidzakhala lanulanu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudzakhala nalo colowa canu wina ndi mnzace yemwe, ndilo limene ndinakwezapo dzanja langa kulipereka kwa makolo anu, ndi dziko ili lidzakugwerani colowa canu.