Ezekiel 47:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Malire ake adzayende motere: chakumpoto kwake achokere ku Nyanja Yaikulu, kutsata mseu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kupitirira ku Zedati,
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku Nyanja Yaikulu, kutsata njira ya ku Hetiloni, kufikira polowera ku Zedadi;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Malire a dzikolo adzakhala motere: Mbali ya kumpoto adzachokera ku Nyanja Yayikulu kutsata msewu wa ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamoti ndi kupitirira ku Zedadi,
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo malire a dzikoli ndi awa: mbali ya kumpoto, kuyambira ku nyanja yaikuru, kutsata njira ya ku Heteloni, kufikira polowera ku Zedadi;