Ezekiel 47:17 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazarenoni umene wachitana malire ndi Damasiko chakumpoto, ndiponso mpaka m'malire a Hamati chakumpoto. Imeneyi ndiyo idzakhala mbali yakumpoto.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi malire ochokera kunyanja ndiwo Hazar-Enoni, kumalire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati. Ndiyo mbali ya kumpoto.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Motero malire akumpoto adzachokera ku nyanja mpaka ku mzinda wa Hazari-Enoni, mʼmalire akumpoto a Damasiko ndi chakumpoto kwa malire a Hamati. Awa adzakhala malire a kumpoto.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi malire ocokera kunyanja ndiwo Hazaremoni, ku malire a Damasiko, ndi kumpoto kulinga kumpoto kuli malire a Hamati, Ndiyo mbali ya kumpoto.