Ezekiel 47:18 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Malire akuvuma ayende chakumwera kuchokera ku Hazarenoni pakati pa Haurani ndi Damasiko, kutsata mtsinje wa Yordani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israele, kuloza ku nyanja yakuvuma mpaka ku Tamara. Imeneyi idzakhala mbali yakuvuma.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Giliyadi, ndi dziko la Israele, ndiwo Yordani; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali ya kummawa malire adzayenda pakati pa Haurani ndi Damasiko, mbali ya ku Yorodani pakati pa Giliyadi ndi dziko la Israeli, ku nyanja ya kummawa mpaka ku mzinda wa Tamara. Awa adzakhala malire akummawa.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mbali ya kum'mawa pakati pa Haurani, ndi Damasiko, ndi Gileadi, ndi dziko la Israyeli, ndiwo Yordano; muyese kuyambira malire a kumpoto kufikira nyanja ya kum'mawa. Ndiyo mbali ya kum'mawa.