Ezekiel 47:19 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Malire akumwera ayende kuchokera ku Tamara mpaka ku dziŵe la Meriboti-Kadesi. Kuchokera kumeneko atsate malire a ku Ejipito mpaka ku Nyanja Yaikulu. Imeneyi ndiyo mbali yakumwera.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi mbali ya kumwera kuloza kumwera ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meribati-Kadesi, ku mtsinje wa Ejipito, ndi ku Nyanja Yaikulu. Ndiyo mbali ya kumwera kuloza kumwera.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Mbali yakummwera malire adzayenda kuchokera ku dziwe la mzinda wa Tamara mpaka ku madzi a ku Meriba Kadesi. Kenaka ndi kutsata chigwa cha ku Igupto mpaka ku Nyanja Yayikulu. Awa adzakhala malire akummwera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi mbali ya kumwela kuloza kumwela ndiyo kuyambira ku Tamara kufikira ku madzi a Meriboti Kadesi, ku mtsinje wa Aigupto, ndi ku nyanja yaikuru. Ndiyo mbali ya kumwela kuloza kumwela.