Ezekiel 47:2 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Adanditulutsira pa chipata chakumpoto, nazungulira nane panja pake mpaka ku chipata chakunja choyang'ana kuvuma. Ndipo ndidaona madzi akutuluka chakumwera kwa chipata.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Pamenepo anatuluka nane njira ya kuchipata cha kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kunka kuchipata chakunja, njira ya kuchipata choloza kum'mawa; ndipo taonani, panatuluka madzi pa mbali ya kulamanja.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ananditulutsira pa chipata chakumpoto ndipo anazungulira nane panja mpaka ku chipata chakunja choyangʼana kummawa. Ndipo ndinaona madzi akutuluka chakummwera kwa chipatacho.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Pamenepo anaturuka nane njira ya ku cipata ca kumpoto, nazungulira nane njira yakunja kumka ku cipata cakunja, njira ya ku cipata coloza kum'mawa; ndipo taonani, panaturuka madzi pa mbali ya kulamanja.