Ezekiel 47:22 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Muligaŵe kuti likhale choloŵa chanu. Likhalenso la alendo amene amakhala pakati panu, nabereka ana pakati panu. Alendowo adzakhala nanu ngati mbadwa za mu Israele. Adzapatsidwa choloŵa chao pamodzi ndi inuyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzachitika kuti muligawe ndi kuchita maere, likhale cholowa chanu, ndi cha alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israele, alandire cholowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israele.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Muligawe kuti likhale cholowa chanu ndiponso cholowa cha alendo amene akukhala pakati panu, nakhala ndi ana pakati panu. Inu muwatenge monga mbadwa za mu Israeli. Adzapatsidwe cholowa chawo pamodzi ndi inu pakati pa mafuko a Israeli.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzacitika kuti muligawe ndi kucita maere, likhale colowa canu, ndi ca alendo akukhala pakati pa inu; ndipo akhale kwa inu ngati obadwa m'dziko mwa ana a Israyeli, alandire colowa pamodzi ndi inu mwa mafuko a Israyeli.