Ezekiel 47:9 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumene mtsinjewo ukuyenda, cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo, nsombanso zidzachuluka. Pakuti madzi ameneŵa amapita kumeneko kuti akometse madzi anzake. Ndipo kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda, zonse zidzakhala ndi moyo.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zochuluka zidzakhala ndi moyo kulikonse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzachuluka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kulikonse mtsinje ufikako zilizonse zidzakhala ndi moyo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Kulikonse kumene mtsinjewo ukuyenda cholengedwa chilichonse chidzakhala ndi moyo. Nsombanso zidzakhala zambiri. Paja madzi amenewa amapita kumeneko kuti akakometse madzi ena. Choncho kulikonse kumene madziwa akuyenda chilichonse chidzakhala ndi moyo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo kudzatero kuti zamoyo zonse zocuruka zidzakhala ndi moyo kuti konse mtsinjewo ufikako, ndi nsomba zidzacuruka kwambiri; pakuti madzi awa anafikako, nakonzeka madzi a m'nyanja; ndipo kuli konse mtsinje ufikako ziri zonse zidzakhala ndi moyo.