Ezekiel 48:1 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Naŵa maina a mafuko: kuyambira ku malire akumpoto kuchokera ku nyanja, kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazarenoni, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyang'anana ndi Hamati, ndipo kuchokera kuvuma mpaka kuzambwe, nchigawo chimodzi, ndipo ncha Dani.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Hetiloni, polowera ku Hamati, Hazara-Enani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zake zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Nawa mayina a mafuko a Israeli: Dani adzakhala ndi chigawo chimodzi kuyambira kumalire akumpoto kuchokera ku nyanja kudzera ku Hetiloni mpaka ku chipata cha Hamati, kukafika ku Hazari-Enani, mzinda umene uli kumpoto kwa malire a Damasiko oyangʼanana ndi Hamati, kuchokera mʼchigawo chimodzi kummawa mpaka kumadzulo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Maina a mafuko tsono ndi awa: Kuyambira nsonga ya kumpoto, ku mbali ya njira ya ku Heteloni, polowera ku Hamati, Hazarenani ku malire a Damasiko kumpoto, ku mbali ya ku Hamati; ndi mbali zace zilinge kum'mawa ndi kumadzulo; Dani akhale nalo gawo limodzi.