Ezekiel 48:10 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigawocho chigaŵidwe motere: chigawo cha Ansembe chikhale cha makilomita 12 ndi theka kumpoto. Kuzambwe chikhale cha makilomita khumi. Kuvuma chikhale cha makilomita asanu. Kumwera chikhale cha makilomita 12 ndi theka. Malo a Nyumba ya Chauta akhale pakatimpakati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo m'mwemo mudzakhala chopereka chopatulika cha ansembe kumpoto, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, ndi kumadzulo mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kum'mawa mikono zikwi khumi kupingasa kwake, ndi kumwera mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake; ndi pakati pake pakhale malo opatulika a Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Ichi chidzakhala chigawo chopatulika cha ansembe ndipo chidzagawidwe motere: Mbali ya kumpoto kutalika kwake kudzakhala makilomita khumi ndi awiri ndi theka, mbali ya kumadzulo kudzakhala makilomita asanu, mbali ya kummawa makilomita asanu ndiponso makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali yakummwera. Pakati pake padzakhala malo a Nyumba ya Mulungu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo m'mwemo mudzakhala copereka copatulika ca ansembe kumpoto, zikwi makumi awiri mphambu zisanu a m'litali mwace, ndi kumadzulo zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kum'mawa zikwi khumi kupingasa kwace, ndi kumwela zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace; ndi pakati pace pakhale malo opatulika a Yehova.