Ezekiel 48:11 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chimenechi chikhale chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene adamvera malamulo anga, osatsata Aisraele pamene adaasokera, monga m'mene adaachitira Alevi.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chimenechi chidzakhala chigawo cha ansembe opatulika, ana a Zadoki, amene ndi okhulupirika ponditumikira Ine, ndipo sanasochere ngati momwe anachitira Alevi pamene Aisraeli anasochera.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Cidzakhala ca ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israyeli, ndi muja anasokera Alevi.