Ezekiel 48:12 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigawo chimenechi, pakati pa zigawo zonse, chidzakhale mphatso yapadera kwa ansembewo, ndipo chikhale chopatulika kwambiri. Chichitane malire ndi dziko la Alevi.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi chiperekocho chikhale chao chotapa pa chopereka cha dziko, ndicho chopatulika kwambiri pa malire a Alevi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawochi, mwa zigawo zonse za mʼdzikomo, chidzakhala kwa ansembewo ngati mphatso yawo yapadera. Chidzachita malire ndi dziko la Alevi.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi ciperekoco cikhale cao cotapa pa copereka ca dziko, ndico copatulikitsa pa malire a Alevi.