Ezekiel 48:15 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Chigawo chotsala muufupi mwake chikhale cha makilomita aŵiri ndi hafu, m'litali mwake makilomita 12 ndi theka. Chikhale malo omangapo mzinda ndiponso busa. Mzinda ukhale pakatimpakati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwake, chakuno cha mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za ntchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Chigawo chotsala mulifupi mwake makilomita awiri ndi theka ndipo mulitali mwake makilomita khumi ndi awiri ndi theka, chidzakhala malo a anthu wamba, chomangapo nyumba ndiponso chodyetsera ziweto zawo. Mzinda udzamangidwa pomwepo ndipo udzakhala pakati ndi pakati.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo zikwi zisanu zotsalazo m'kupingasa kwace, cakuno ca zikwi makumi awiri mphambu zisanu, zikhale za nchito wamba za mudzi, za kumangapo zapabusa; ndi mudzi ukhale pakati pace.