Ezekiel 48:16 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Miyeso yake ikhale iyi: Kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 2,250. Kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 2,250.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndi miyeso yake ndi iyi: mbali ya kumpoto, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwera, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kum'mawa, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Miyeso yake ndi iyi: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 2,250, kummwera mamita 2,250, kummawa mamita 2,250 ndipo kumadzulo mamita 2,250.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndi miyeso yace ndi iyi: mbali ya kumpoto, mabango zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumwela, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kummawa, zikwi zinai mphambu mazana asanu; ndi mbali ya kumadzulo, zikwi zinai mphambu mazana asanu.