Ezekiel 48:17 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dera la busa likhale motere: kumpoto kutalika kwake kukhale mamita 125. Kumwera kutalika kwake kukhale mamita 125. Kuvuma kutalika kwake kukhale mamita 125. Ndipo kuzambwe kutalika kwake kukhale mamita 125.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lake; kumpoto mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwera mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mikono mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mikono mazana awiri mphambu makumi asanu.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo cha mzinda chodyetsera ziweto chidzakhala motere: kumpoto kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummwera kutalika kwake kudzakhala mamita 125, kummawa kutalika kwake kudzakhala mamita 125, ndipo kumadzulo kutalika kwake kudzakhala mamita 125.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo mudziwo ukhale ndi busa lace; kumpoto mabango mazana awiri mphambu makumi asanu, kumwela mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kum'mawa mazana awiri mphambu makumi asanu, ndi kumadzulo mazana awiri mphambu makumi asanu.