Ezekiel 48:18 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Chigawo chotsala pafupi ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu kuvuma, makilomita asanu kuzambwe. Chikhale dziko la minda ya anthu ogwira ntchito mu mzinda.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo madera otsalawo m'litali mwake alingane ndi chopereka chopatulika, ndicho mikono zikwi khumi kum'mawa, ndi mikono zikwi khumi kamadzulo, alingane ndi chopereka chopatulika; ndi zipatso zake zikhale za chakudya cha iwo ogwira ntchito m'mudzi.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo chotsala, choyandikana ndi chigawo chopatulika, kutalika kwake makilomita asanu mbali yakummawa ndiponso makilomita asanu mbali ya kumadzulo. Dera limeneli lidzakhale lolimamo anthu ogwira ntchito mu mzinda.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo madera otsalawo m'litali mwace alingane ndi copereka copatulika, ndico zikwi khumi kum'mawa, ndi zikwi khumi kumadzulo, alingane ndi copereka copatulika; ndi zipatso zace zikhale za cakudya ca iwo ogwira nchito m'mudzi.