Ezekiel 48:20 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Tsono chigawo chathunthu chopatulikacho chikhale cha makilomita 12 ndi theka mbali zonse, ndiye kuti chigawo chopatulikacho pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Chopereka chonse ndicho mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwake, mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwake; muchipereke chopereka chopatulika chaphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
Chigawo chopatulika chonsechi chidzakhale makilomita khumi ndi awiri ndi theka mbali zonse. Ndiye kuti, mudzapatule padera chigawo chopatulika pamodzi ndi kadziko ka mzindawo.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Copereka conse ndico mabango zikwi makumi awiri mphambu zisanu m'litali mwace, zikwi makumi awiri mphambu zisanu kupingasa kwace; mucipereke copereka copatulika camphwamphwa, pamodzi ndi dziko la mudziwo.