Ezekiel 48:21 — Compare Translations

4 translations compared side by side

Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
“Tsono chigawo chotsala pa mbali zonse ziŵiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuvuma, mbali ina kuyambiranso m'malire a chigawo chopatulika kukalekeza m'malire akuzambwe, kumapaza kufupi ndi zigawo za mafuko, dera lonselo likhale la mfumu. Chigawo chopatulika ndi malo oyera a Nyumba ya Mulungu zikhale pakatimpakati.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali ina ndi ina ya chopereka chopatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu za chopereka kumalire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa mikono zikwi makumi awiri mphambu zisanu kumalire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo cha kalonga; ndipo chopereka chopatulika ndi malo opatulika a Kachisi zidzakhala pakati pake.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Tsono chigawo chotsala pambali zonse ziwiri za chigawo chopatulika ndi za kadziko ka mzinda, chikhale cha mfumu. Chidzayenda motere: kuyambira mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera mʼmalire akummawa. Mbali ina kuyambiranso mʼmalire a chigawo chopatulika kukalekezera malire a kumadzulo, kudutsa kufupi ndi zigawo za mafuko. Dera lonselo likhale la mfumu.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ndipo madera ena otsalawo ndiwo a kalonga, mbali yina ndi yina ya copereka copatulika ndi ya dziko la mudzi, kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu za copereka ku malire a kum'mawa, ndi kumadzulo kutsogolo kwa zikwi makumi awiri mphambu zisanu ku malire a kumadzulo, pandunji pa magawo enawo ndiwo ca kalonga; ndipo copereka copatulika ndi malo opatulika a kacisi zidzakhala pakati pace.