Ezekiel 48:29 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Dziko lonselo ndilo mupatse mafuko a Israele kuti likhale choloŵa chao. Zigawo zimenezi zidzakhala zao. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israele ndi kuchita maere, likhale cholowa chao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Ili ndilo dziko limene mudzagawire mafuko a Israeli kuti likhale cholowa. Zimenezi zidzakhala zigawo zawo, ndikutero Ine Ambuye Yehova.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
Ili ndi dziko muligawire mafuko a Israyeli ndi kucita maere, likhale colowa cao; ndipo awa ndi magawo ao, ati Ambuye Yehova.