Ezekiel 48:33 — Compare Translations
4 translations compared side by side
Chewa (Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa)
Kumwera, kumene kutalika kwake ndi kwa mamita 2,250, kukhale ndi zipata zitatu: chipata cha Simeoni, cha Isakara ndi cha Zebuloni.
Chewa 1922 (Buku Lopatulika)
ndi kumbali ya kumwera ayese mikono zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: chipata chimodzi cha Simeoni, chipata chimodzi cha Isakara, chipata chimodzi cha Zebuloni;
Chewa 2002 (Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero)
“Mbali yakummwera, imene kutalika kwake ndi mamita 2,250, kudzakhala zipata zitatu izi: chipata cha Simeoni, chipata cha Isakara ndi chipata cha Zebuloni.
Chewa Bible (BL) 1992 - Buku Lopatulika
ndi ku mbali ya kumwela ayese zikwi zinai mphambu mazana asanu, ndi zipata zitatu: cipata cimodzi ca Simeoni, cipata cimodzi ca Isakara, cipata cimodzi ca Zebuloni;